Posts

Dziko Lonse Likulira: Papa Francis Wamwalira

Image
Lero dziko lonse likulirira. Mtumiki wathu, mtumwi wa mtendere, mtsogoleri wa Tchalitchi cha Katolika Papa Francis   wamwalira ali ndi zaka 88 . Nkhaniyi yatsimikizidwa ndi Vatican m'mawa uno, ndipo ikufalikira mofulumira padziko lonse lapansi. Papa Francis  Papa Francis, anabadwa ngati Jorge Mario Bergoglio ku Argentina, anali Papa woyamba kuchokera ku America, komanso wa mtundu wa Jesuit. Kuyambira atasankhidwa mu March 2013 , anasankha dzina Francis osati chifukwa chokopa, koma kuti akhale ngati Mtumiki wa osauka St. Francis of Assisi . Sanali Papa wa mphamvu anali Papa wa mtima . Anakana kukhala m'nyumba zokongola za Vatican, ndipo anasankha kukhala m'chipinda chaching'ono chisonyezo cha moyo wake wopanda kudzikuza. Papa Francis anali wolimba mtima. Anayankhula za kusintha kwa nyengo (climate change), kusasiyana kwa olemera ndi osauka, kulandira othawa kwawo, komanso za chikondi cha Mulungu kwa aliyense – ngakhale amene ena amawawona ngati osayenera. Anati: “...

Zigawenga zazikwanje azigamula kukakhala ku ndende ku Lilongwe

Image
Khrisimasi yomwe inali yoti izakhale yachisomo ndi chisangalalo inasanduka usiku wadzidzidzi ku Area 46, pomwe gulu la anthu osakonda malamulo linaukira banja limodzi m’nyumba yawo, ndithu kukhala usiku womwe sadzaiwala. Pakali pano, Khothi la Senior Resident Magistrate ku Lilongwe lagamula amuna anayi kukhala ku ndende zaka zosiyanasiyana atapezeka olakwa pa mlandu wokhudzana ndi kuba mwachiwawa komanso kuvulaza ana ndi alendo. A Yohane Daniel a zaka 26  ndi Evance Lufeyo a zaka 39  adalandira chilango chachikulu cha zaka 20 , pamene Dickson Mavuto a zaka 30  awalandira zaka 13 ndipo Madalitso Soniyala a zaka 37  awalamula kukhala m’ndende kwa zaka 18 . Zigawenga za zikwanje Mneneri wa polisi ku Lilongwe, a Hastings Chigalu , anafotokoza kuti pa 25 December usiku, anthuwo limodzi ndi zigawenga zawo zopitilira khumi, anaukira nyumba ya banja lina ku Area 46 ali ndi zikwanje ndi zida zina zowopsa . Atathyola chitseko, adalamula anthu m’nyumbamo kupereka mafoni, ...

Mnyamata wa Zaka 18 Agamulidwa Zaka 14 ku Ndende pa Chiwembu cha Kuba ku Gateway Mall

Image
Mu mlandu wochititsa mantha, bwalo la milandu ku Lilongwe lagamula mnyamata wa zaka 18 dzina lake James Gerald kuti akakhale ku ndende kwa zaka 14 chifukwa chobera munthu ndalama zokwana K40,000, foni, komanso katundu wina wokwana pafupifupi K1 miliyoni. James Gerald ndi katundu yemwe adaba Izi zidachitika pa 1 February chaka chino, pafupi ndi malo okwerera mabasi pa Gateway Mall. Malingana ndi Khumbo Sanyiwa, wachiwiri kwa mneneri wa apolisi ku Lilongwe, bwalo lidamva kuti Gerald pamodzi ndi anzake awiri omwe akusakidwa anachita chiwembuchi ali ndi zikwanje ndipo anaukira munthu pa nthawi ya 4 koloko madzulo. Woimira boma pa mlanduwu, Damiano Nyasulu, anauza bwalo kuti atatuwo anamutengera munthu katundu wake mwamphamvu komanso molimbikitsidwa ndi zida zowopsa. James Gerald amachokera m’mudzi wa Tsikulamowa, T/A Tsikulamowa, m’chigawo cha Ntcheu. Kulingalira kwa bwalo lino ndikutenga gawo lalikulu polimbana ndi umbanda, makamaka mwa achinyamata omwe akuchulukira kuchita zauchigawe...

Doc Wafika Ku Mangochi – Ma Ambulance ayende basi!

Image
Ayi izi nde zikuyenda! Kumbukirani kale pomwe Doc analonjeza kuti ma ambulance amene "anafafa ngati nsomba pa dzuwa" adzawauka? Eeee, tsopano tiyeni tikupatseni nkhani yatsopano Doc wafika ku Mangochi! Ndiye abaleeee… madongosolo ayamba kukung’anitsidwa ngati msewu wa Area 18! Dr. Namadingo ku Mangochi Koma Akuluakulu Achipatala Atathawa! Lero Doc wafika ponyezimira ku Mangochi koma akuluakulu achipatala atathawa kale ngati anawamva kuti Doc akubwera! Zina mwa izi sizikudziwika, koma Doc wati, "Nde zili bwino, ndagona kuno lero." Madongosolo Kudzutsa Ma Ambulance Oyimilira Ngati Ma Statue Mawa tikuyembekezera kuti akangokumana ndi atsogoleriwo (mwina pamene ali pa tea break ), ndiye njira zidzayamba kukonzedwa. Ma ambulance amene anali ngati amangodikira kuvala thonje m’kamwa adzayambanso kuuluka pa msewu ngati galimoto ya wedding! Ma Shirt A White? Kodi Ndi Campaign Izi? Doc wanyamulanso ma shirt a white angapo zikuoneka ngati akufuna anthu adziwe kuti ...

Malonda a Fodya Aimitsidwa ku Msika wa Limbe: Alimi Akwiya ndi Mtengo Wotsikitsitsa

Image
  Msika wa fodya ku Limbe wayimitsidwa kwakanthawi pambuyo poti alimi ambiri adadzudzula mtengo wotsika wa fodya, womwe ukufika pa $1.15 pa kilo. Alimi ati mtengo uwu ndi wopweteka chifukwa sufanana ndi ndalama zomwe adagwiritsa ntchito polima fodya kuchokera ku munda. Msika wafodya wa Limbe Alimi ambiri amati ntchito yawo ya chaka chonse, kuphatikiza ndalama zogulira feteleza, mankhwala, ndi ntchito yolima, sizikuoneka ngati zikulipidwa moyenera ndi mtengo umene akupezawu. "Tikuvutika kwambiri. Tilimi tikuyika ndalama zambiri komanso nthawi yochuluka mu ulimiwu, koma pamapeto pake sitikupeza chilungamo," anatero mlimi wina m’modzi amene timacheza naye. Mandala, itapita ku msika wa Limbe, idapeza kuti mtengo wokwera kwambiri wa fodya wogulitsidwa mpaka pano wafika pa $3.20 pa kilo. Komabe, izi zikuoneka ngati zikusiyana kwambiri ndi mtengo wamba wa $1.15, zomwe zikuchititsa kuti alimi ambiri asakhutitsidwe. Zikuoneka kuti pali kusiyana kwakukulu pakati pa zomwe alimi akuy...

Kaliati Akuti Usi Wapepera – Koma Mandala Yapeza Zina!

Image
  Mabodza kapena zoona? Nkhani yatsopano yowotchera m’ndale ya Malawi yafika pa desk la Mandala , ndipo sitingangodutsa popanda kukufikitsirani chilichonse mwatsatanetsatane. Pa msonkhano wachipani cha UTM womwe wachitika ku Blantyre, mtsogoleri wachipani amenenso ndi wachipwitikizi pazolankhula, Patricia Kaliati , adanenetsa kuti Dr. Micheal Usi wapeperadi kwa UTM. Iye adati Usi analankhula ndi Dalitso Kabambe , ndipo anavomereza kuti anachita zolakwa kuchoka mchipanichi ndipo tsopano akufuna kubwerera. Patricia Kaliati ndi achitetezo ku Blantyre  Koma Mandala sanangomva nkhaniyi tafufuza! Tatalowa m’mbali ya gulu Odya Zake Alibe Mulandu , ndipo Happy Kondowe , mlembi wamkulu wa gululi, watsutsa molimba zimene Kaliati wanena. “ A Usi sanapepese konse kwa UTM ,” adatero Kondowe polankhula ndi Mandala. “Anangokumana ndi a Kabambe ku maliro ku Phalombe. Ndipo panalibe zokhudza chipani zomwe zidanenedwa.” Dalitso Kabambe ndi Michael Usi ku Phalombe Iye anapitilira kunena ku...

Zokoma Zatembenuka: Wa Arsenal, George Nkhoma, Apezeka Wolakwa pa Chigololo ndi Mwana wa Zaka 13 – Agamulidwa Zaka 14 Ku Ndende!

Image
  Koma ayi! Mdzulo uno nkhani yati bwii kuchokera ku Nkhunga First Grade Magistrate ku Dwangwa, Nkhotakota, yapangitsa anthu kuseka ndi kulira nthawi imodzi. George Nkhoma, wazaka 26  komanso supporter wamkulu wa Arsenal , walowa mu line-up ya omwe akakhala ku bench ya ndende kwa zaka 14 chifukwa cha kugonana ndi mwana wamkazi wa zaka 13. Eish, ngati mukanakhala pa Premier League mukanangopatsidwa red card yomweyo! George Nkhoma  Malingana ndi mboni ya boma, Mickeas Chatsira (omwe mwina pano ndi VAR wa milandu), zinthu zoyipa zinayamba mu November chaka chatha mpaka mu March chaka chino. George, mwachikondi chobisika koma choipa, ankachotsa chilakolako pa mwana yemwe sanakwanitse ngakhale zaka 14. Kodi zimenezi zinali zachibwana? Ai, zinali za tactics ! A George, chifukwa cha “man-management” yawo ya coach wa chikondi chosavomerezeka, anafika povumbulutsa foni ya makono (smartphone) kwa mwanayu kuti azilumikizana naye mosavuta ngati Pep Guardiola atagula striker wa...

Zachisoni ku Lupachi: Mnyamata wa Zaka 19 wazipha Ndi Mfuti

Image
  Mu tawuni ya Lupachi, yomwe ili pa malire a Mzimba ndi Nkhotakota, padachitika tsoka lalikulu lomwe lasiya mabanja ndi anthu ambiri m'mbali mwa chisoni. A Tone Nyirongo, mnyamata wa zaka 19, wachosa moyo wake powombera mutu ndi mfuti mu nyumba mwake. Malingana ndi a Macfarlen Mseteka, omwe ndi mneneri wa Polisi ya Jenda, chigawochi chidachitika dzulo, nthawi imene a Nyirongo adangouza m'bale wake kuti akonzekere kukolola nyemba m'munda mwake nthawi ikakwana. Zinthu zidawoneka ngati zili bwino, koma zinali zoyambira tsanziko loyamba la moyo wake. Patadutsa nthawi yochepa atachoka, banja lake lidamva kulira kwa mfuti kuchokera mu nyumba, ndipo atalowa kukaona zimene zachitika, adapeza a Nyirongo wazipha. Zikuwoneka kuti nkhani yokolola nyemba inali njira yokonzekera kutsanzika ulendo owopsa wa kudzipha. Zochitika ngati izi zikukumbutsa anthu ambiri kufunikira kokambirana nkhani za maganizo ndi nkhawa. Polisi akumangokumbutsa anthu kuti akamva kuti akupsinjika m'maga...

Popular posts from this blog

Mfumu Yaikulu Gawa Undi Aletsa Magule Opanda Ulemu pa Kulamba 2025

Ngozi ya Sitima ya M'madzi ku Likoma: Atatu afa, ena asanu ndi atatu apulumutsidwa

Nkhani Yachisoni ku Mchinji: Bambo wamangidwa Atapha Mwana Wake Chifukwa Chosamvera