Dziko Lonse Likulira: Papa Francis Wamwalira

Image
Lero dziko lonse likulirira. Mtumiki wathu, mtumwi wa mtendere, mtsogoleri wa Tchalitchi cha Katolika Papa Francis   wamwalira ali ndi zaka 88 . Nkhaniyi yatsimikizidwa ndi Vatican m'mawa uno, ndipo ikufalikira mofulumira padziko lonse lapansi. Papa Francis  Papa Francis, anabadwa ngati Jorge Mario Bergoglio ku Argentina, anali Papa woyamba kuchokera ku America, komanso wa mtundu wa Jesuit. Kuyambira atasankhidwa mu March 2013 , anasankha dzina Francis osati chifukwa chokopa, koma kuti akhale ngati Mtumiki wa osauka St. Francis of Assisi . Sanali Papa wa mphamvu anali Papa wa mtima . Anakana kukhala m'nyumba zokongola za Vatican, ndipo anasankha kukhala m'chipinda chaching'ono chisonyezo cha moyo wake wopanda kudzikuza. Papa Francis anali wolimba mtima. Anayankhula za kusintha kwa nyengo (climate change), kusasiyana kwa olemera ndi osauka, kulandira othawa kwawo, komanso za chikondi cha Mulungu kwa aliyense – ngakhale amene ena amawawona ngati osayenera. Anati: “...

Kaliati Akuti Usi Wapepera – Koma Mandala Yapeza Zina!

 


Mabodza kapena zoona? Nkhani yatsopano yowotchera m’ndale ya Malawi yafika pa desk la Mandala, ndipo sitingangodutsa popanda kukufikitsirani chilichonse mwatsatanetsatane.

Pa msonkhano wachipani cha UTM womwe wachitika ku Blantyre, mtsogoleri wachipani amenenso ndi wachipwitikizi pazolankhula, Patricia Kaliati, adanenetsa kuti Dr. Micheal Usi wapeperadi kwa UTM. Iye adati Usi analankhula ndi Dalitso Kabambe, ndipo anavomereza kuti anachita zolakwa kuchoka mchipanichi ndipo tsopano akufuna kubwerera.

Patricia Kaliati ndi achitetezo ku Blantyre 

Koma Mandala sanangomva nkhaniyi tafufuza!

Tatalowa m’mbali ya gulu Odya Zake Alibe Mulandu, ndipo Happy Kondowe, mlembi wamkulu wa gululi, watsutsa molimba zimene Kaliati wanena.

A Usi sanapepese konse kwa UTM,” adatero Kondowe polankhula ndi Mandala. “Anangokumana ndi a Kabambe ku maliro ku Phalombe. Ndipo panalibe zokhudza chipani zomwe zidanenedwa.”

Dalitso Kabambe ndi Michael Usi ku Phalombe
Iye anapitilira kunena kuti Micheal Usi alibe ganizo lililonse lobwerera ku UTM, komanso sadatsutsane ndi lingaliro lawo loti a Kabambe anachotsedwa chifukwa chawo mu UTM.

Zotsutsana poyera

Tsono apa zinthu zikusonyeza zotsutsana. Mbali imodzi, UTM ikuti Usi akufuna kubwerera, ndipo mbali inayo, anthu oyandikana naye akuti ndithu ayi.

Kodi UTM ikufuna kuoneka ngati ikukopa anthu obwerera, kapena pali ndale za m’kati zomwe zikusewera? Kapena bwanji nkhaniyi yachititsidwa kufuna kutchuka kwa chipani pa nthawi ya chisankho?

Mandala ikutsatira zonse!

Izi sizomaliza, ndipo monga mwazolowera, Mandala sidzasiya kufufuza chilichonse chimene chili chowona. Sitinadzuke lero, ndipo sitingadzalale. Tikhala pambuyo pa nkhaniyi mpaka itatuluka zonse.

Inu mukuti bwanji? Kodi Usi abwerera ku UTM? Kapena Kaliati akungolankhula za zoti zisakhalepo? Lekani comment yanu pansipa, ndipo musaiwale kutsatira Mandala kuti mudziwe zonse zatsopano zomwe ena safuna mudziwe!

Comments

Popular posts from this blog

Mfumu Yaikulu Gawa Undi Aletsa Magule Opanda Ulemu pa Kulamba 2025

Ngozi ya Sitima ya M'madzi ku Likoma: Atatu afa, ena asanu ndi atatu apulumutsidwa

Nkhani Yachisoni ku Mchinji: Bambo wamangidwa Atapha Mwana Wake Chifukwa Chosamvera