Dziko Lonse Likulira: Papa Francis Wamwalira

Image
Lero dziko lonse likulirira. Mtumiki wathu, mtumwi wa mtendere, mtsogoleri wa Tchalitchi cha Katolika Papa Francis   wamwalira ali ndi zaka 88 . Nkhaniyi yatsimikizidwa ndi Vatican m'mawa uno, ndipo ikufalikira mofulumira padziko lonse lapansi. Papa Francis  Papa Francis, anabadwa ngati Jorge Mario Bergoglio ku Argentina, anali Papa woyamba kuchokera ku America, komanso wa mtundu wa Jesuit. Kuyambira atasankhidwa mu March 2013 , anasankha dzina Francis osati chifukwa chokopa, koma kuti akhale ngati Mtumiki wa osauka St. Francis of Assisi . Sanali Papa wa mphamvu anali Papa wa mtima . Anakana kukhala m'nyumba zokongola za Vatican, ndipo anasankha kukhala m'chipinda chaching'ono chisonyezo cha moyo wake wopanda kudzikuza. Papa Francis anali wolimba mtima. Anayankhula za kusintha kwa nyengo (climate change), kusasiyana kwa olemera ndi osauka, kulandira othawa kwawo, komanso za chikondi cha Mulungu kwa aliyense – ngakhale amene ena amawawona ngati osayenera. Anati: “...

Ngozi ya Sitima ya M'madzi ku Likoma: Atatu afa, ena asanu ndi atatu apulumutsidwa

 

Usiku wa dzulo, ngozi yochititsa mantha idachitika pa madzi a Nyanja ya Malawi m'chigawo cha Likoma, pomwe sitima yaying'ono idamira, n’kupha anthu atatu pomwe ena asanu ndi atatu apulumutsidwa.



Malinga ndi mneneri wa apolisi ku Likoma, Sergeant Enala Kalua, ngoziyi idachitika pamene anthu ankayenda mu bwato laling'ono kuchokera kumtunda kufuna kukwera sitima ya Chilembwe yomwe inali pakati pa nyanja, ikuchoka ku Mangochi kupita ku Nkhata Bay.

Kalua adati, bwato laling’onolo lidamira ndi anthu onsewo ali m'njira yopita kukakwera sitimayo. Panopa apolisi limodzi ndi ogwira ntchito yadzidzidzi akupitiriza kufufuza kuti adziwe chiwerengero chenicheni cha anthu amene anali m'bwatomo komanso amene akusowa mpaka pano.

“Ili ndi tsoka lalikulu, ndipo tikupempha anthu kukhala tcheru akamayenda pa madzi, makamaka pa nyengo ya mphepo kapena madzulo,” Kalua adatero.

Tikutumiza mawu achisoni kwa mabanja a onse omwe ataya okondedwa awo chifukwa cha ngoziyi.

Comments

Popular posts from this blog

Mfumu Yaikulu Gawa Undi Aletsa Magule Opanda Ulemu pa Kulamba 2025

Nkhani Yachisoni ku Mchinji: Bambo wamangidwa Atapha Mwana Wake Chifukwa Chosamvera