Dziko Lonse Likulira: Papa Francis Wamwalira
Pamene mwezi wa August ukukulira, anthu a m'dera la AChewa a Malawi, Zambia ndi Mozambique akuyamba kukonzekera mwambo waukulu wa Kulamba Ceremony womwe umachitikira ku Mkaika, Zambia. Mwambo uwu ndi chionetsero chachikulu cha chikhalidwe cha AChewa, ndipo chaka chino ukuyembekezeka kuchitika pa 30 August 2025.
![]() |
| Gule wa mkulu |
Koma zinthu zasintha pang'ono chaka chino…
Mfumu yayikulu ya AChewa onse, Kalonga Gawa Undi, watsutsa mwamphamvu gule wamkulu wamaliseche komanso omwe amavina molimbana ndi chikhalidwe. Poyankhula nthawi ya zokonzekera mwambo wa chaka chino, Gawa Undi walamula kuti magule onse amene adzatengerepo mbali pa mwambowu azikhala aulemu, osavina kapena kuvala zinthu zomwe zingawononge ulemu wa chikhalidwe cha AChewa.
“Ife AChewa timadziwika ndi ulemu. Tikufuna kuti mwambo wa Kulamba ukhale chionetsero cha chikhalidwe chathu cholemekezeka, osati mwayi wochitira zinthu zosayenera,” watero Gawa Undi.
Mfumu yayikulu Lukwa ya m’boma la Kasungu, yomwe imalunzanitsa ntchito za AChewa a mayiko atatuwa, yatsimikiza kuti uthenga wa Gawa Undi watsitsidwa kale kwa mafumu onse ku Malawi, Zambia ndi Mozambique.
“Chaka chatha panali gule amene anabwezedwa chifukwa chosalemekeza. Gawa akukumbutsa kuti chaka chino zisachitikenso. Tiyeni tisonyeze chikhalidwe chathu chosungika, osati chonyozeka,” watero Mfumu Lukwa.
Zokonzekera za Kulamba zikuyenda bwino. Msonkhano woyamba unachitika pa 29 March ndipo wachiwiri ukuyembekezeka pa 26 April. Zikuwonekeratu kuti chaka chino Kulamba adzakhala mwambo wokumbukiridwa, wokhala ndi magule olemekeza chikhalidwe ndi cholinga cha mwambo.
Tiyeni tonse tipereke chithandizo pa cholinga cha Gawa Undi, kudzibweretsera ulemu ndi kusunga chikhalidwe cha AChewa pa Kulamba 2025!
Comments
Post a Comment