Dziko Lonse Likulira: Papa Francis Wamwalira

Image
Lero dziko lonse likulirira. Mtumiki wathu, mtumwi wa mtendere, mtsogoleri wa Tchalitchi cha Katolika Papa Francis   wamwalira ali ndi zaka 88 . Nkhaniyi yatsimikizidwa ndi Vatican m'mawa uno, ndipo ikufalikira mofulumira padziko lonse lapansi. Papa Francis  Papa Francis, anabadwa ngati Jorge Mario Bergoglio ku Argentina, anali Papa woyamba kuchokera ku America, komanso wa mtundu wa Jesuit. Kuyambira atasankhidwa mu March 2013 , anasankha dzina Francis osati chifukwa chokopa, koma kuti akhale ngati Mtumiki wa osauka St. Francis of Assisi . Sanali Papa wa mphamvu anali Papa wa mtima . Anakana kukhala m'nyumba zokongola za Vatican, ndipo anasankha kukhala m'chipinda chaching'ono chisonyezo cha moyo wake wopanda kudzikuza. Papa Francis anali wolimba mtima. Anayankhula za kusintha kwa nyengo (climate change), kusasiyana kwa olemera ndi osauka, kulandira othawa kwawo, komanso za chikondi cha Mulungu kwa aliyense – ngakhale amene ena amawawona ngati osayenera. Anati: “...

Zokoma Zatembenuka: Wa Arsenal, George Nkhoma, Apezeka Wolakwa pa Chigololo ndi Mwana wa Zaka 13 – Agamulidwa Zaka 14 Ku Ndende!

 


Koma ayi! Mdzulo uno nkhani yati bwii kuchokera ku Nkhunga First Grade Magistrate ku Dwangwa, Nkhotakota, yapangitsa anthu kuseka ndi kulira nthawi imodzi. George Nkhoma, wazaka 26  komanso supporter wamkulu wa Arsenal, walowa mu line-up ya omwe akakhala ku bench ya ndende kwa zaka 14 chifukwa cha kugonana ndi mwana wamkazi wa zaka 13. Eish, ngati mukanakhala pa Premier League mukanangopatsidwa red card yomweyo!

George Nkhoma 

Malingana ndi mboni ya boma, Mickeas Chatsira (omwe mwina pano ndi VAR wa milandu), zinthu zoyipa zinayamba mu November chaka chatha mpaka mu March chaka chino. George, mwachikondi chobisika koma choipa, ankachotsa chilakolako pa mwana yemwe sanakwanitse ngakhale zaka 14.

Kodi zimenezi zinali zachibwana? Ai, zinali za tactics! A George, chifukwa cha “man-management” yawo ya coach wa chikondi chosavomerezeka, anafika povumbulutsa foni ya makono (smartphone) kwa mwanayu kuti azilumikizana naye mosavuta ngati Pep Guardiola atagula striker watsopano!

Pa nthawi ya milandu, George anapempha kuti apatsidwe yellow card osati red card poti, iye anati zomwe zinachitika “inali mistake chabe.” Mistake? Monga kudula buluku osavula nsapato! Koma bwalo silinamve zimenezo, linangoti straight red card out for 14 years!

M’mene akulowa mu ndende, akuti amalira osati chifukwa cha chilango ayi koma chifukwa Arsenal yatha mwayi wa title mu EPL. Zina zonse zili ndi time-table, koma Champions League ya ndende? Palibe transfer window.

Tingonena kuti Mlalawo kumene George amachokera tsopano wakhala wotchuka. Koma si chifukwa cha maize, ayi, koma chifukwa cha Gunner wopita kundende!

Chiphunzitso?
Tikakhala pa offside m’mbali ya malamulo, tikangopeza ban nthawi iliyonse. Ana ndi atsogolo osawaseweretsa ngati mpira wa Premier League. Ndipo a George, next time uzikonda Arsenal yokha, osati ana a primary!

Masewera a chikondi ali ndi malamulo awo. George wapita ku camp. Tiyeni tikhale a VAR m'moyo wathu!

Comments

Popular posts from this blog

Mfumu Yaikulu Gawa Undi Aletsa Magule Opanda Ulemu pa Kulamba 2025

Ngozi ya Sitima ya M'madzi ku Likoma: Atatu afa, ena asanu ndi atatu apulumutsidwa

Nkhani Yachisoni ku Mchinji: Bambo wamangidwa Atapha Mwana Wake Chifukwa Chosamvera