Dziko Lonse Likulira: Papa Francis Wamwalira
Ayi izi nde zikuyenda! Kumbukirani kale pomwe Doc analonjeza kuti ma ambulance amene "anafafa ngati nsomba pa dzuwa" adzawauka? Eeee, tsopano tiyeni tikupatseni nkhani yatsopano Doc wafika ku Mangochi! Ndiye abaleeee… madongosolo ayamba kukung’anitsidwa ngati msewu wa Area 18!
![]() |
| Dr. Namadingo ku Mangochi |
Koma Akuluakulu Achipatala Atathawa!
Lero Doc wafika ponyezimira ku Mangochi koma akuluakulu achipatala atathawa kale ngati anawamva kuti Doc akubwera! Zina mwa izi sizikudziwika, koma Doc wati, "Nde zili bwino, ndagona kuno lero."
Madongosolo Kudzutsa Ma Ambulance Oyimilira Ngati Ma Statue
Mawa tikuyembekezera kuti akangokumana ndi atsogoleriwo (mwina pamene ali pa tea break), ndiye njira zidzayamba kukonzedwa. Ma ambulance amene anali ngati amangodikira kuvala thonje m’kamwa adzayambanso kuuluka pa msewu ngati galimoto ya wedding!
Ma Shirt A White? Kodi Ndi Campaign Izi?
Doc wanyamulanso ma shirt a white angapo zikuoneka ngati akufuna anthu adziwe kuti "ndiine amene ndikukonzanso zinthu!" Tiyeni tiyembekezere ngati sipadzakhala ma cap, ma wristband, ndi ma poster!
Tikulira Ndi Chimwemwe – Ma Ambulance Kubwerera Ku Moyo!
Apa nde zinthu zikuyenda! Ma ambulance akadzuka, odwala sadzayenda ndi matola kapena bajaji opanda shock absorber. Tidzawona zinthu zikubwezeredwa pa track ngakhale ma siren akuyimba wee wee ngati nyimbo ya weekend!
Doc anavaya! Big man Namadingo!
Comments
Post a Comment