Dziko Lonse Likulira: Papa Francis Wamwalira

Image
Lero dziko lonse likulirira. Mtumiki wathu, mtumwi wa mtendere, mtsogoleri wa Tchalitchi cha Katolika Papa Francis   wamwalira ali ndi zaka 88 . Nkhaniyi yatsimikizidwa ndi Vatican m'mawa uno, ndipo ikufalikira mofulumira padziko lonse lapansi. Papa Francis  Papa Francis, anabadwa ngati Jorge Mario Bergoglio ku Argentina, anali Papa woyamba kuchokera ku America, komanso wa mtundu wa Jesuit. Kuyambira atasankhidwa mu March 2013 , anasankha dzina Francis osati chifukwa chokopa, koma kuti akhale ngati Mtumiki wa osauka St. Francis of Assisi . Sanali Papa wa mphamvu anali Papa wa mtima . Anakana kukhala m'nyumba zokongola za Vatican, ndipo anasankha kukhala m'chipinda chaching'ono chisonyezo cha moyo wake wopanda kudzikuza. Papa Francis anali wolimba mtima. Anayankhula za kusintha kwa nyengo (climate change), kusasiyana kwa olemera ndi osauka, kulandira othawa kwawo, komanso za chikondi cha Mulungu kwa aliyense – ngakhale amene ena amawawona ngati osayenera. Anati: “...

Malonda a Fodya Aimitsidwa ku Msika wa Limbe: Alimi Akwiya ndi Mtengo Wotsikitsitsa

 


Msika wa fodya ku Limbe wayimitsidwa kwakanthawi pambuyo poti alimi ambiri adadzudzula mtengo wotsika wa fodya, womwe ukufika pa $1.15 pa kilo. Alimi ati mtengo uwu ndi wopweteka chifukwa sufanana ndi ndalama zomwe adagwiritsa ntchito polima fodya kuchokera ku munda.

Msika wafodya wa Limbe

Alimi ambiri amati ntchito yawo ya chaka chonse, kuphatikiza ndalama zogulira feteleza, mankhwala, ndi ntchito yolima, sizikuoneka ngati zikulipidwa moyenera ndi mtengo umene akupezawu. "Tikuvutika kwambiri. Tilimi tikuyika ndalama zambiri komanso nthawi yochuluka mu ulimiwu, koma pamapeto pake sitikupeza chilungamo," anatero mlimi wina m’modzi amene timacheza naye.

Mandala, itapita ku msika wa Limbe, idapeza kuti mtengo wokwera kwambiri wa fodya wogulitsidwa mpaka pano wafika pa $3.20 pa kilo. Komabe, izi zikuoneka ngati zikusiyana kwambiri ndi mtengo wamba wa $1.15, zomwe zikuchititsa kuti alimi ambiri asakhutitsidwe.

Zikuoneka kuti pali kusiyana kwakukulu pakati pa zomwe alimi akuyembekezera ndi zomwe msika ukupereka. Pofuna kupewa mavuto ena, oyang’anira msika wa Limbe adaganiza zoimitsa malonda kwakanthawi kuti akambirane ndi anthu okhudzidwa.

Nthawi ikuwonetsa kuti pofuna kukulitsa chuma cha mlimi, pali kufunika kokonza momwe fodya amagulitsidwira komanso kuwonetsetsa kuti alimi akulandira mtengo woyenerera ndi wolingana ndi ntchito yawo.

Tiyeni tipitirize kutsatira nkhaniyi kuti tidziwe zomwe zidzachitike mtsogolo pa msika wa fodya ku Limbe.

#Fodya #LimbeMarket #UlimiWoyenerera #MalondaAmisika

Comments

Popular posts from this blog

Mfumu Yaikulu Gawa Undi Aletsa Magule Opanda Ulemu pa Kulamba 2025

Ngozi ya Sitima ya M'madzi ku Likoma: Atatu afa, ena asanu ndi atatu apulumutsidwa

Nkhani Yachisoni ku Mchinji: Bambo wamangidwa Atapha Mwana Wake Chifukwa Chosamvera