Dziko Lonse Likulira: Papa Francis Wamwalira

Image
Lero dziko lonse likulirira. Mtumiki wathu, mtumwi wa mtendere, mtsogoleri wa Tchalitchi cha Katolika Papa Francis   wamwalira ali ndi zaka 88 . Nkhaniyi yatsimikizidwa ndi Vatican m'mawa uno, ndipo ikufalikira mofulumira padziko lonse lapansi. Papa Francis  Papa Francis, anabadwa ngati Jorge Mario Bergoglio ku Argentina, anali Papa woyamba kuchokera ku America, komanso wa mtundu wa Jesuit. Kuyambira atasankhidwa mu March 2013 , anasankha dzina Francis osati chifukwa chokopa, koma kuti akhale ngati Mtumiki wa osauka St. Francis of Assisi . Sanali Papa wa mphamvu anali Papa wa mtima . Anakana kukhala m'nyumba zokongola za Vatican, ndipo anasankha kukhala m'chipinda chaching'ono chisonyezo cha moyo wake wopanda kudzikuza. Papa Francis anali wolimba mtima. Anayankhula za kusintha kwa nyengo (climate change), kusasiyana kwa olemera ndi osauka, kulandira othawa kwawo, komanso za chikondi cha Mulungu kwa aliyense – ngakhale amene ena amawawona ngati osayenera. Anati: “...

Mnyamata wa Zaka 18 Agamulidwa Zaka 14 ku Ndende pa Chiwembu cha Kuba ku Gateway Mall


Mu mlandu wochititsa mantha, bwalo la milandu ku Lilongwe lagamula mnyamata wa zaka 18 dzina lake James Gerald kuti akakhale ku ndende kwa zaka 14 chifukwa chobera munthu ndalama zokwana K40,000, foni, komanso katundu wina wokwana pafupifupi K1 miliyoni.

James Gerald ndi katundu yemwe adaba

Izi zidachitika pa 1 February chaka chino, pafupi ndi malo okwerera mabasi pa Gateway Mall. Malingana ndi Khumbo Sanyiwa, wachiwiri kwa mneneri wa apolisi ku Lilongwe, bwalo lidamva kuti Gerald pamodzi ndi anzake awiri omwe akusakidwa anachita chiwembuchi ali ndi zikwanje ndipo anaukira munthu pa nthawi ya 4 koloko madzulo.

Woimira boma pa mlanduwu, Damiano Nyasulu, anauza bwalo kuti atatuwo anamutengera munthu katundu wake mwamphamvu komanso molimbikitsidwa ndi zida zowopsa.

James Gerald amachokera m’mudzi wa Tsikulamowa, T/A Tsikulamowa, m’chigawo cha Ntcheu. Kulingalira kwa bwalo lino ndikutenga gawo lalikulu polimbana ndi umbanda, makamaka mwa achinyamata omwe akuchulukira kuchita zauchigawenga.

Apolisi akupitiliza kufunafuna anzake awiri omwe akuthawa, ndipo akupempha anthu omwe angakhale ndi chidziwitso chilichonse chingathandize kuti agwire omwe akuthawawo.

Comments

Popular posts from this blog

Mfumu Yaikulu Gawa Undi Aletsa Magule Opanda Ulemu pa Kulamba 2025

Ngozi ya Sitima ya M'madzi ku Likoma: Atatu afa, ena asanu ndi atatu apulumutsidwa

Nkhani Yachisoni ku Mchinji: Bambo wamangidwa Atapha Mwana Wake Chifukwa Chosamvera