Dziko Lonse Likulira: Papa Francis Wamwalira
Msika wa Chinamwali mu mzinda wa Zomba wasanduka ngati malo osiyira zinyalala. Kwa mwezi wathunthu tsopano, khonsolo ya mzindawu sinachotse zinyalala zomwe zikungokulirakulira tsiku ndi tsiku.
Malinga ndi Kanfosi Jalisi, m'modzi mwa amalonda omwe amagulitsa ku msikawu, vutoli layamba kuwonetsa kuti litha kubweretsa matenda chifukwa cha kusowa ukhondo. "Zinyalala zikuchuluka, ndipo tilibe chitetezo chaumoyo. Anthu amatha kudwala ndipo ife amalonda timavutika kugwira ntchito m'malo osachita bwino atero," anatero Jalisi, amene sanabisenso kukhumudwa kwake.
Iye anafotokozanso kuti amalonda a m'msika wa Chinamwali opitilira 1,500 alankhula kuti akagwiritsa ntchito ndalama zawo zokha kuchotsa zinyalala ngati khonsoloyi sipereka chithandizo. "Timapereka ndalama zambiri pa tsiku, koma sitikuona ntchito yeniyeni yachitukuko m'msikamu. Bola tisiye kupereka ndalamazo ndipo tilembe galimoto yathu kuchotsa nyasizi," adatero Jalisi.
Mbali ya khonsolo, mkulu wa bungweli a Archangel Bakolo komanso Mfumu ya mzindawu a Christopher Jana, avomereza kuti vuto lilipo. Iwo ati ena mwa magalimoto omwe amachotsa zinyalala aonongeka ndipo pakali pano akudikira kuti akonzedwe.
"Koma izi sizikutanthauza kuti sitikupeza njira. Panopa tapeza kampani yomwe ikugwira ntchito yochotsa zinyalalazi pakadali pano, pomwe tikukonza magalimoto athu ena," atero a Jana.
Zikuwoneka kuti nthawi yofuna kusintha yakwana. Amalonda akufuna khonsolo ichite zambiri kuposa kungolandira ndalama. Ndipo ngati zinthu sizisintha, mwina adzatenga zinthu m'manja mwawo mwachitsanzo, kulemba galimoto yawo yochotsa zinyalala.
Kodi izi zikusonyeza kusasamala kwa mabungwe a boma? Kapena ndi kusowa kwa zinthu zofunikira monga magalimoto? Chifukwa chilichonse chili choncho, amalonda a Chinamwali sakufuna kukhala chete. Tsopano ndi nthawi yoti mphamvu ya amalonda imveke.
Comments
Post a Comment