Dziko Lonse Likulira: Papa Francis Wamwalira

Image
Lero dziko lonse likulirira. Mtumiki wathu, mtumwi wa mtendere, mtsogoleri wa Tchalitchi cha Katolika Papa Francis   wamwalira ali ndi zaka 88 . Nkhaniyi yatsimikizidwa ndi Vatican m'mawa uno, ndipo ikufalikira mofulumira padziko lonse lapansi. Papa Francis  Papa Francis, anabadwa ngati Jorge Mario Bergoglio ku Argentina, anali Papa woyamba kuchokera ku America, komanso wa mtundu wa Jesuit. Kuyambira atasankhidwa mu March 2013 , anasankha dzina Francis osati chifukwa chokopa, koma kuti akhale ngati Mtumiki wa osauka St. Francis of Assisi . Sanali Papa wa mphamvu anali Papa wa mtima . Anakana kukhala m'nyumba zokongola za Vatican, ndipo anasankha kukhala m'chipinda chaching'ono chisonyezo cha moyo wake wopanda kudzikuza. Papa Francis anali wolimba mtima. Anayankhula za kusintha kwa nyengo (climate change), kusasiyana kwa olemera ndi osauka, kulandira othawa kwawo, komanso za chikondi cha Mulungu kwa aliyense – ngakhale amene ena amawawona ngati osayenera. Anati: “...

Zifukwa Zomwe Alimi Ayenera Kulima Mbeu Zopilira Ku Ng'amba – Malangizo Ochokera ku Makoka Research Farm


Dzulo ku Makoka Research Farm, yomwe kale inkatchedwa Makoka Research Station, ku Zomba kunachitika chionetsero chachikulu cha ulimi. Pa mwambowu, alimi anauzidwa kuti nthawi yakwana yoti asiye kulima mwachizolowezi ndipo ayambe kugwiritsa ntchito njira zamakono, makamaka kulima mbeu zopilira ku ng'amba.

Alimi aku Zomba

A Jessie Mvula, Wogwira Ntchito ku Makoka Research Farm, anati mbeu monga mbatata, nthochi, mapira, soya, komanso chimanga cha makono zikhoza kubweretsa zokolola zambiri ngati alimi atatsatira malangizo a ulimi moyenera. Iye anafotokoza kuti limodzi mwa zolinga zawo ndi kulumikiza alimi ndi makampani kuti azitha kugulitsa zokolola zawo pa mitengo yabwino. Izi zingathandize alimi kukhala ndi chakudya chokwanira komanso ndalama m'matumba mwawo.

Jessie Mvula

A Mvula anawonjezera kuti:

“Tili okonzeka kumalumikizitsa alimi ndi makampani kuti azikagulitsa zokolola zawo kumeneko pa mitengo yabwino.”

Bungwe la Center for Agricultural Transformation (CAT) lomwe lidatsogolera chionetserocho, kudzera mwa mkulu wake a McLeod Nkhoma, linatsindika kuti alimi sayenera kungodalira kulima kokha, koma azigwiritsa ntchito njira zamakono monga ulimi wa nthilira komanso kugwiritsa ntchito matekinoloje ena a luso.

Nyakwawa Ndechere, pansi pa Senior Chief Mlumbe, adati kudzera m'misonkhano yomwe akhala akuchititsa, akulimbikitsa anthu awo kuti asiye njira zakale zosabala bwino, ndipo atembenuke mtima kulimbikira ulimi wamakono womwe uli ndi phindu lalikulu.

Zimene Tinga Phunzire:

1. Kulima mbeu zopilira ku ng’amba kuli ndi phindu lalikulu.

2. Kugwiritsa ntchito njira zamakono monga ulimi wa nthilira kumakulitsa zokolola.

3. Alimi ayenera kulumikizana ndi makampani kuti apeze misika yabwino.

4. Bungwe la CAT likugwira ntchito yolimbikitsa chisinthe cha njira za ulimi.

Nthawi yakwana yoti ulimi ukhale gwero la chuma chenicheni. Tiyeni tichite kusintha!


Comments

Popular posts from this blog

Mfumu Yaikulu Gawa Undi Aletsa Magule Opanda Ulemu pa Kulamba 2025

Ngozi ya Sitima ya M'madzi ku Likoma: Atatu afa, ena asanu ndi atatu apulumutsidwa

Nkhani Yachisoni ku Mchinji: Bambo wamangidwa Atapha Mwana Wake Chifukwa Chosamvera