Dziko Lonse Likulira: Papa Francis Wamwalira

Image
Lero dziko lonse likulirira. Mtumiki wathu, mtumwi wa mtendere, mtsogoleri wa Tchalitchi cha Katolika Papa Francis   wamwalira ali ndi zaka 88 . Nkhaniyi yatsimikizidwa ndi Vatican m'mawa uno, ndipo ikufalikira mofulumira padziko lonse lapansi. Papa Francis  Papa Francis, anabadwa ngati Jorge Mario Bergoglio ku Argentina, anali Papa woyamba kuchokera ku America, komanso wa mtundu wa Jesuit. Kuyambira atasankhidwa mu March 2013 , anasankha dzina Francis osati chifukwa chokopa, koma kuti akhale ngati Mtumiki wa osauka St. Francis of Assisi . Sanali Papa wa mphamvu anali Papa wa mtima . Anakana kukhala m'nyumba zokongola za Vatican, ndipo anasankha kukhala m'chipinda chaching'ono chisonyezo cha moyo wake wopanda kudzikuza. Papa Francis anali wolimba mtima. Anayankhula za kusintha kwa nyengo (climate change), kusasiyana kwa olemera ndi osauka, kulandira othawa kwawo, komanso za chikondi cha Mulungu kwa aliyense – ngakhale amene ena amawawona ngati osayenera. Anati: “...

Nkhani Yochititsa Mantha ku Dedza: Amuna Awiri Akumangidwa pa Mlandu Wogwiririra ndi Kuba

 

Mudzi wa Bikiele m’boma la Dedza wasokonekera ndi nkhani yochititsa mantha yomwe yachitika sabata ino, pomwe mayi wa zaka 45 akuti adagwiriridwa komanso kulandidwa zinthu zake madzulo a Lolemba ndipo omwe akuganiziridwa kuti achita izi ndi Matthews Malitchi (25) ndi Nyozani Chitukula (24), ndipo pano akusungidwa m’chitokosi cha apolisi ya Dedza.

Malinga ndi malipoti, mayiyu ankachoka kumalo omwe amagulitsirako mowa usiku wa Lolemba, ndipo panjira anagwa m’manja mwa a Malitchi ndi a Chitukula omwe akuganiziridwa kuti anamudzunza mwankhanza.

Mneneri wa apolisi ku Dedza, a Beatrice Jefita, watsimikiza kuti amunawa agwidwa ndipo akuyembekezeka kuoneka ku bwalo lamilandu posachedwapa. Mzimayiyu, yemwe adakumana ndi zowawa, akulandirabe chithandizo pa chipatala chachikulu cha Dedza.

A Malitchi amachokera mmudzi mwa Kaphala, ndipo a Chitukula amachokera mmudzi mwa Chimati, kwa T/A Kaphuka. M'mudzi komanso dera lonse la Dedza, anthu akupempha kuti chilungamo chioneke ndipo mlandu uwu usatengedwe mopepuka.

Tikapita patsogolo ndi nkhaniyi, tikupitiliza kufufuza kuti tiwonetsetse kuti choonadi chikutuluka, ndipo mayiyu apeza chilungamo komanso chithandizo chonse chomwe akuyenera.

Pitilizani kutsatira blog iyi kuti mumve zambiri za momwe nkhaniyi ikuyendera.

Comments

Popular posts from this blog

Mfumu Yaikulu Gawa Undi Aletsa Magule Opanda Ulemu pa Kulamba 2025

Ngozi ya Sitima ya M'madzi ku Likoma: Atatu afa, ena asanu ndi atatu apulumutsidwa

Nkhani Yachisoni ku Mchinji: Bambo wamangidwa Atapha Mwana Wake Chifukwa Chosamvera