Dziko Lonse Likulira: Papa Francis Wamwalira

Image
Lero dziko lonse likulirira. Mtumiki wathu, mtumwi wa mtendere, mtsogoleri wa Tchalitchi cha Katolika Papa Francis   wamwalira ali ndi zaka 88 . Nkhaniyi yatsimikizidwa ndi Vatican m'mawa uno, ndipo ikufalikira mofulumira padziko lonse lapansi. Papa Francis  Papa Francis, anabadwa ngati Jorge Mario Bergoglio ku Argentina, anali Papa woyamba kuchokera ku America, komanso wa mtundu wa Jesuit. Kuyambira atasankhidwa mu March 2013 , anasankha dzina Francis osati chifukwa chokopa, koma kuti akhale ngati Mtumiki wa osauka St. Francis of Assisi . Sanali Papa wa mphamvu anali Papa wa mtima . Anakana kukhala m'nyumba zokongola za Vatican, ndipo anasankha kukhala m'chipinda chaching'ono chisonyezo cha moyo wake wopanda kudzikuza. Papa Francis anali wolimba mtima. Anayankhula za kusintha kwa nyengo (climate change), kusasiyana kwa olemera ndi osauka, kulandira othawa kwawo, komanso za chikondi cha Mulungu kwa aliyense – ngakhale amene ena amawawona ngati osayenera. Anati: “...

Mulandu wa a Dr. Cassium Chilumpha ofuna kupha Bingu wa Muthalika ukupitirira


Lero ku Blantyre, Bwalo la Milandu lapereka malangizo ofunikira pa mlandu wa Dr. Cassium Chilumpha, yemwe akuzengedwa mlandu wokhudza chinyengo cha kufuna kupha pulezidenti wakale Bingu wa Mutharika. Iyi ndi nkhani yomwe yakhala ikukambidwa kwa nthawi yaitali kuyambira mu 2006 momwe Dr. Chilumpha anamangidwa.

Dr. Cassium Chilumpha
Ma Jaji atatu, Bruno Kalemba, Charlotte Malonda, ndi Justus Kishindo omwe akuyang’anira mlanduwu, aitanira m’mbali zonse za mlandu kuti apereke zolemba za mfundo zawo mkati mwa masiku khumi ndi anai (14). Izi zikuchitika pokonzekera kuti bwalo la milandu liyambe kumva mlanduwu pa 17 June, chaka chino.

Loya wa Dr. Chilumpha, a Kalekeni Kaphale, atulutsa chidziwitso chakuti lero bwalo la milandu lakhala likumvetsera momwe mlanduwu uyendere, ndipo palibe zomwe zayamba kumvedwa zokhudza umboni weniweni.

Zodabwitsa ndi zakuti mlanduwu wakhala ukuchedwa kwambiri, chinthu chomwe chadzetsa kudandaula kuchokera kwa anthu osiyanasiyana kuphatikizapo ma loya ake a Dr. Chilumpha. Kuyambira nthawi yomwe anamangidwa mu 2006, pali kusowa kwa chitukuko pa nkhaniyi, ndipo anthu ambiri akufuna kuona chilungamo pa nkhaniyi kaya Dr. Chilumpha ndi wolakwa kapena ayi.

Pakadali pano, anthu akungoyembekezera tsiku lomwe mlanduwu uyambe kuweruzidwa ndi kupeza mayankho omveka pa mlandu wautaliwu.

Zikomo Powerenga, khalani tcheru kuti mumve zambiri zokhudza nkhaniyi pamene ikupita patsogolo osaiwala kupanga comment ndikupanga follow.

Comments

Popular posts from this blog

Mfumu Yaikulu Gawa Undi Aletsa Magule Opanda Ulemu pa Kulamba 2025

Ngozi ya Sitima ya M'madzi ku Likoma: Atatu afa, ena asanu ndi atatu apulumutsidwa

Nkhani Yachisoni ku Mchinji: Bambo wamangidwa Atapha Mwana Wake Chifukwa Chosamvera