Dziko Lonse Likulira: Papa Francis Wamwalira
Pa bwalo la milandu la Magistrate, lero kwachitika zachilendo pomwe mlandu wa a Alfred Gangata, wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha DPP ku Central Region, wachititsa chisokonezo.
![]() |
| Alfred Gangata ndi anthu ena |
Izi zachitika chifukwa oweruza a Austin Banda alamula kuti a mbali ya boma akalembenso bwinobwino mfundo za mlanduwo (zomwe zimadziwika kuti "particulars of the offence") chifukwa sizinasonyeze bwino kuti a Gangata akuwazenga mlandu wanji.
A Gangata akuwaganizira kuti anapeza satifiketi ya fomu folo mwachinyengo, ndipo pakadali pano ali pa belo ndipo lero anapita kubwalo la milandu kuti akavomere kapena kuukana mlanduwu. Koma ndondomekoyi sinatheke chifukwa a mbali yoyankhapo mlandu anabweretsa mtsutso wokhudza mmene mfundo za mlanduwo zalembedwera.
Oimira boma, a Charles Panyani, anatsutsana ndi zimenezi, akutsindika kuti mfundo za mlanduwo zalembedwa bwinobwino. Komabe, oweruza a Banda sanavomereze izi, ndipo analamula kuti mlanduwo ulembedwe kuchokera poyambiranso, ndi kufotokoza bwinobwino zolakwa zomwe akuwaganizira a Gangata.
Lamulo ili likutanthauza kuti mlandu wa a Gangata wachoka pa siteji yomwe ankayembekezera kuti athane nawo mwachindunji, ndipo tsopano akuyembekezera kuti boma libweretse milandu yomwe ili yomveka komanso yolemekezeka molingana ndi malamulo.
Zikuwonekeratu kuti milandu ikafika ku bwalo, si nkhani yokungoyambitsa basi, koma lemba lililonse, ndime iliyonse, komanso tanthauzo lake zimakhala zofunika kwambiri.
Tiyeni tiwone momwe nkhaniyi iyendere m’masiku akubwerawa.
Comments
Post a Comment