Dziko Lonse Likulira: Papa Francis Wamwalira

Image
Lero dziko lonse likulirira. Mtumiki wathu, mtumwi wa mtendere, mtsogoleri wa Tchalitchi cha Katolika Papa Francis   wamwalira ali ndi zaka 88 . Nkhaniyi yatsimikizidwa ndi Vatican m'mawa uno, ndipo ikufalikira mofulumira padziko lonse lapansi. Papa Francis  Papa Francis, anabadwa ngati Jorge Mario Bergoglio ku Argentina, anali Papa woyamba kuchokera ku America, komanso wa mtundu wa Jesuit. Kuyambira atasankhidwa mu March 2013 , anasankha dzina Francis osati chifukwa chokopa, koma kuti akhale ngati Mtumiki wa osauka St. Francis of Assisi . Sanali Papa wa mphamvu anali Papa wa mtima . Anakana kukhala m'nyumba zokongola za Vatican, ndipo anasankha kukhala m'chipinda chaching'ono chisonyezo cha moyo wake wopanda kudzikuza. Papa Francis anali wolimba mtima. Anayankhula za kusintha kwa nyengo (climate change), kusasiyana kwa olemera ndi osauka, kulandira othawa kwawo, komanso za chikondi cha Mulungu kwa aliyense – ngakhale amene ena amawawona ngati osayenera. Anati: “...

Khansala Wakale wa Naming’azi, Willy M’manga, Ayikidwa Mmanda Mawa

 


M’dera la Naming’azi mu Zomba Malosa Constituency, anthu akulira ndi maliro a khansala wakale Willy M’manga yemwe anali membala wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP). A M’manga amwalira posachedwapa pa Chipatala Chachikulu cha Zomba, komwe amalandira chithandizo cha matenda a shuga.

Willy M'manga

Willy M’manga anali munthu wodziwika komanso wolemekezeka m’dziko lake, ndipo anatumikira bwino anthu a m’dera la Naming’azi pa nthawi yomwe anali khansala.

Malinga ndi wapampando wa khonsolo ya Zomba, Khansala Brazio Chinthenga, thupi la khansala M’manga liyikidwa mmanda mawa, Lamlungu, m’dera la kwawo ku Naming’azi. A Chinthenga atsimikiza za imfayi ndipo ati banja limodzi ndi khonsolo apereka zambiri zokhudza dongosolo la maliro.

Pamene anthu a ku Naming’azi akukonzekera kumupereka kwa ambuye khansala wakale, ambiri akukumbukira ntchito yake yabwino komanso chikondi chimene anali nacho pa dera lake. Pumulani mumtendere a Willy M’manga.

Comments

Popular posts from this blog

Mfumu Yaikulu Gawa Undi Aletsa Magule Opanda Ulemu pa Kulamba 2025

Ngozi ya Sitima ya M'madzi ku Likoma: Atatu afa, ena asanu ndi atatu apulumutsidwa

Nkhani Yachisoni ku Mchinji: Bambo wamangidwa Atapha Mwana Wake Chifukwa Chosamvera