Dziko Lonse Likulira: Papa Francis Wamwalira

Image
Lero dziko lonse likulirira. Mtumiki wathu, mtumwi wa mtendere, mtsogoleri wa Tchalitchi cha Katolika Papa Francis   wamwalira ali ndi zaka 88 . Nkhaniyi yatsimikizidwa ndi Vatican m'mawa uno, ndipo ikufalikira mofulumira padziko lonse lapansi. Papa Francis  Papa Francis, anabadwa ngati Jorge Mario Bergoglio ku Argentina, anali Papa woyamba kuchokera ku America, komanso wa mtundu wa Jesuit. Kuyambira atasankhidwa mu March 2013 , anasankha dzina Francis osati chifukwa chokopa, koma kuti akhale ngati Mtumiki wa osauka St. Francis of Assisi . Sanali Papa wa mphamvu anali Papa wa mtima . Anakana kukhala m'nyumba zokongola za Vatican, ndipo anasankha kukhala m'chipinda chaching'ono chisonyezo cha moyo wake wopanda kudzikuza. Papa Francis anali wolimba mtima. Anayankhula za kusintha kwa nyengo (climate change), kusasiyana kwa olemera ndi osauka, kulandira othawa kwawo, komanso za chikondi cha Mulungu kwa aliyense – ngakhale amene ena amawawona ngati osayenera. Anati: “...

Alonda Awiri a Times Ku Lilongwe Amangidwa ndi Apolisi Poti Akuganiziridwa Kuba Mafuta a Galimoto

 


M’dziko lathu muli nthano zambiri zokhudza kuba, koma iyi imachititsa chidwi kwambiri chifukwa inachitika ku ofesi ya nyuzipepala yotchuka ya Times ku Lilongwe. Apolisi ku Lilongwe amanga alonda awiri ogwira ntchito ku Times chifukwa akuganiziridwa kuti anaba mafuta a galimoto usiku wa Lachitatu.

Mneneri wa apolisi a Hastings Chigalu, adatsimikizira kuti alonda awiriwo ndi a Aubrey Whitman, wa zaka 25, ndi a Amin Cassim, wa zaka 36. A Chigalu adati awiriwa anapopa mafuta a galimoto okwana 10 litres kuchokera mgalimoto ina ya kampaniyo ndipo anachita izi asadziwe kuti ofesiyo ili ndi kamera za chitetezo zomwe zinalemba zonse zomwe anachita.

Aubrey Whitman & Amin Cassim

Kamera zinawonetsa momwe awiriwa anapoperamo mafutawo ndikuwatsitsa mu zigubu, kenako kugwiritsa ntchito jumbo kutulutsa mafutawo mgalimoto. Kodi zomwe anachita zinali ndi cholinga chotani?

Chodabwitsa kwambiri n’chakuti m’mawa wa tsikulo, nthawi ya 4 koloko, mlonda mmodzi adanyamula zigubu zija ndikufuna kupita kukagulitsa mafutawo kunja. Koma choyipa chinamupeza asanafike patali – ana oyendayenda m’tauni ya Lilongwe anamumanga ndikumuberanso mafutawo omwewo.

Tsopano, nkhani iyi yasiya anthu ambiri akudabwa: Kodi kuthekera kwa kukhala ndi makamera ku ntchito kungateteze bwanji katundu wa kampani? Nanga kodi tikhulupilira ndani ngati anthu omwe akuyenera kuteteza katundu ndiye akuba?

Zikomo kuti mukuwerenga – ngati muli ndi maganizo pa nkhaniyi, musazengereze kuyankhapo mu comment section!

Comments

Post a Comment

Popular posts from this blog