Dziko Lonse Likulira: Papa Francis Wamwalira
Elisa Balakasi, mwamuna wa zaka 40, wagamulidwa zaka 9 kundende chifukwa chogwiririra mwana wake wamkazi wazaka 14 yobadwa.
![]() |
| Elisa Balakasi |
A Balakasi adagonana ndi mwana wawo mu mwezi wa February, pomwe Balakasi ananyengerera mwanayi ndi ndalama zokwana K5000 asanachite naye zadamazi patchire pafupi ndi nyumba yawo. Nkhaniyi inatuluka mwezi wa March, mwana atayamba kuonetsa zizindikiro zoti ali ndi pakati. Amayi ake atafunsa, mwanayo adawulula zowawa zomwe zinamuchitikira, ndipo nkhaniyi inaperekedwa ku polisi ya Namizana.
Woimira boma pa mlandu, a Thokozani Moloko, adalongosola nkhaniyi m'bwalo la milandu la ku Mchinji, ndipo mneneri wa polisi a Limbani Mpinganjira adatsimikiziranso nkhaniyi kwa anthu.
Ataima m’bwalo la milandu, Balakasi adapempha kulandira chilango chochepa ponena kuti mavuto a m’banja ndi amene adamukakamiza kuchita zimenezo. Koma oweruza a Juma Chilowetsa sanamvepo kanthu ka chisoni. Iwo anati, “Mlandu ngati uwu wachuluka kwambiri m’dziko muno, ndi chifukwa chake chilango chiyenera kukhala chokhwima.”
Balakasi amachokera ku mudzi mwa Nyakwawa, m’dera la mfumu yayikulu Mavwere ku Mchinji.
Comments
Post a Comment