Dziko Lonse Likulira: Papa Francis Wamwalira

Image
Lero dziko lonse likulirira. Mtumiki wathu, mtumwi wa mtendere, mtsogoleri wa Tchalitchi cha Katolika Papa Francis   wamwalira ali ndi zaka 88 . Nkhaniyi yatsimikizidwa ndi Vatican m'mawa uno, ndipo ikufalikira mofulumira padziko lonse lapansi. Papa Francis  Papa Francis, anabadwa ngati Jorge Mario Bergoglio ku Argentina, anali Papa woyamba kuchokera ku America, komanso wa mtundu wa Jesuit. Kuyambira atasankhidwa mu March 2013 , anasankha dzina Francis osati chifukwa chokopa, koma kuti akhale ngati Mtumiki wa osauka St. Francis of Assisi . Sanali Papa wa mphamvu anali Papa wa mtima . Anakana kukhala m'nyumba zokongola za Vatican, ndipo anasankha kukhala m'chipinda chaching'ono chisonyezo cha moyo wake wopanda kudzikuza. Papa Francis anali wolimba mtima. Anayankhula za kusintha kwa nyengo (climate change), kusasiyana kwa olemera ndi osauka, kulandira othawa kwawo, komanso za chikondi cha Mulungu kwa aliyense – ngakhale amene ena amawawona ngati osayenera. Anati: “...

MA ARV AYAMBA KUSOWA MU MALAWI

Anthu pafupifupi 1 million (936,480) mdziko muno ali pachiopsezo chosowa mankhwala otalikitsa moyo a ma ARV ngati dziko la America lipitilire ndi ganizo losiya kupereka thandizo lomwe limadzera Ku bungwe la Presidents Emergency Plan for Aids Relief (PEPFAR).

Izi ndimalinga ndi zomwe lanena bungwe la amFAR lomwe limapanga kafukufuku komanso kuthandizira ntchito zolimbana ndi matenda a AIDS komanso kachirombo ka HIV.

Malinga ndi lipotili Malawi ndi dziko limodzi lomwe likhudzidwe pa anthu opyora 20 million pa dziko lonse omwe amapindura ndi thandizo la Ma ARV kudzera mu PEPFAR.

President Donald Trump wa dziko la America analamula kuti mabungwe adzikolo omwe akugwira ntchito zachifundo mayiko ena asiye kaye kugwira ntchito kwa miyezi itatu.

Comments

Popular posts from this blog

Mfumu Yaikulu Gawa Undi Aletsa Magule Opanda Ulemu pa Kulamba 2025

Ngozi ya Sitima ya M'madzi ku Likoma: Atatu afa, ena asanu ndi atatu apulumutsidwa

Nkhani Yachisoni ku Mchinji: Bambo wamangidwa Atapha Mwana Wake Chifukwa Chosamvera