Dziko Lonse Likulira: Papa Francis Wamwalira
Thyolo, dziko lathu lokoma lino, silimalephera kutipatsa nkhani zomwe zingakupangitseni kuseka ngakhale mutavutika ndi njala yomwe chimanga chachitiridwachi. Lero tili ndi nkhani yomwe ikungofunika chinthu chimodzi chokha: popcorn, chifukwa iyi ndi drama ya "matumba 10 a chimanga" yomwe ingapose ngakhale series ya Money Heist!
Kodi zachitika bwanji?
Chinachitika n’choti boma linali pa mission yabwino—kupereka chimanga kwa anthu omwe akuvutika ndi njala ku Ntambanyama, m’boma la Thyolo. Galimoto yodzaza ndi matumba 700 a chimanga inanyamuka ngati momwe zimayendera nthawi zambiri... koma apa, zinthu zinapota ngati sitiroko yatsopano ya WhatsApp.
M’galimoto munali dalaivala, mulonda wa khonsolo dzina lake Aubrey Malindi, ndi munthu wina wotchedwa Leonard Jika, wazaka 39, yemwe amagwira ntchito ngati wothandizira wa dalaivalayo. Tsono anthu awa m'malo moti azingopereka chimangacho monga momwe zinalili pa plan, anaganiza zochita business yosadziwika m’malemba a khonsolo. Yes! Private sector at its worst!
Iwo ananyamuka ndi chimanga chonse kupita ku Ntambanyama, koma apa ndiye amakhala ngati aikuletsa GPS. Kufika pa msewu, analowetsa mode ya “business unusual”, ndi kuyamba kugulitsa matumba khumi a chimanga kwa mavenda m’mbali mwa msewu—ngati ali pa pulogalamu ya Buy One, Feed None.
Koma anthu sanangoyang’ana chabe.
Zinthu zinali ngati filimu. Anthu akaona chimanga cha boma chikugulitsidwa m'manja mwa vendors, anayamba kuchita investigation mode. Zotsatira zake? Azibambo athuwo anathawa galimoto ngati ikulipuka – kuisiyira pakati pa msewu, pofuna kuti apulumuke ndi miyoyo yawo. Komabe sizinatheke. Apolisi a Thyolo anachita mwachangu—kugwira a Malindi ndi a Jika ngati mchenga wa pa nyanja.
Dalaivala? Watha ngati bowa m’nkhalango.
Apa ndiye nkhani yasintha! Ngakhale chimanga cha matumba 10 chatayika, malipoti a khonsolo akuti chimanga chonse – 700 bags – sichinasowe. Eya, boma lakana kulandira loss report. Matumbawo ndi okwanira. Nanga 10 aja? Mwina anali sample packs kapena "promo packs" monga momwe amakonda kunena m'masitolo akulu akulu.
Chondiphunzitsa ife apa n’chakuti:
Ngati mukugwira ntchito yosamalira chimanga cha boma, musayese kuchita short-cut yopita ku Ntambanyama kudzera m’misewu ya vending business. Boma liri ndi maso, anthu ali ndi makutu, ndipo apolisi ali ndi ma handcuffs omwe sali pa budget koma amapezeka nthawi zonse.
Tidzawona momwe nkhaniyi itathere, koma kwa pano, tikungoti: ndalama zatha, chimanga chapita, koma drama ndiye yatsala!
Siyani maganizo Anu Kuma comment
Comments
Post a Comment